1 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
2 Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
3 zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
4 Sitidzabisira ana awo,
5 Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo
6 kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,
7 Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu
8 Iwo asadzakhale monga makolo awo,
9 Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta,
10 iwo sanasunge pangano la Mulungu
11 Anayiwala zimene Iye anachita,
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,
18 Ananyoza Mulungu mwadala
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,
20 Iye atamenya thanthwe
21 Yehova atawamva anakwiya kwambiri;
22 pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu
23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba
24 anagwetsa mana kuti anthu adye,
25 Anthu anadya buledi wa angelo,
26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba,
27 Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi,
28 Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo,
29 Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka
30 Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho,
31 mkwiyo wa Mulungu unawayakira;
32 Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa;
33 Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya.
34 Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo;
35 Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo,
36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo,
37 Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye,
38 Komabe Iye anali wachifundo;
39 Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe,
40 Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu
41 Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu;
42 Sanakumbukire mphamvu zake,
43 tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto,
44 Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi;
45 Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga,
46 Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala,
47 Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala
48 Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala,
49 Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo,
50 Analolera kukwiya,
51 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;
53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha
54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo
56 Koma iwo anayesa Mulungu
57 Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo,
58 Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano;
59 Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri;
60 Anasiya nyumba ya ku Silo,
61 Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo,
62 Anapereka anthu ake ku lupanga;
63 Moto unanyeketsa anyamata awo,
64 ansembe awo anaphedwa ndi lupanga,
65 Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo,
66 Iye anathamangitsa adani ake;
67 Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe,
68 Koma anasankha fuko la Yuda,
69 Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda,
70 Anasankha Davide mtumiki wake
71 kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa
72 Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama;