1 Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere,
2 Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi,
3 Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo,
4 Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa;
5 Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake;
6 Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
7 Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru,
8 Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo;
9 Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi;
10 Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha,
11 Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi;
12 Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake
13 Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino,
14 Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi,
15 Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa,
16 Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru
17 Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse,
18 Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole
19 Wokonda zolakwa amakonda mkangano,
20 Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino;
21 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake,
22 Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino,
23 Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri
24 Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru,
25 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake
26 Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa,
27 Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu,
28 Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete;