1 “Masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo,
2 ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse
3 Anagawana anthu anga pochita maere
4 “Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu.
5 Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano.
6 Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.
7 “Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu.
8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
9 Lengezani izi pakati pa anthu a mitundu ina:
10 Sulani makasu anu kuti akhale malupanga
11 Bwerani msanga, inu anthu a mitundu yonse kuchokera ku mbali zonse,
12 “Mitundu ya anthu idzuke;
13 Tengani chikwakwa chodulira tirigu,
14 Chigulu cha anthu, chigulu cha anthu,
15 Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa,
16 Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni
17 “Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wanu,
18 “Tsiku limenelo mapiri adzachucha vinyo watsopano,
19 Koma Igupto adzasanduka bwinja,
20 Koma Yuda adzakhala ndi anthu mpaka muyaya
21 Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululuke