1 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
2 Monga momwe moto umatenthera tchire
3 Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
4 Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
5 Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
6 Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
7 Palibe amene amapemphera kwa Inu
8 Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
9 Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?