Números 29
NYA vs NTLH
1 “ ‘Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Ili ndi tsiku limene muziliza malipenga.
1 O Senhor deu a Moisés as seguintes ordens para o povo de Israel: — No dia primeiro do sétimo mês vocês se reunirão para adorar o
2 Muzipereka mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi wopanda chilema monga nsembe zopsereza, fungo lokoma kwa Yehova.
2 Ofereçam a Deus, o Senhor , um sacrifício que será completamente queimado, que tem um cheiro agradável a ele. Esse sacrifício será de um touro novo, um carneiro e sete carneirinhos de um ano, todos sem defeito.
3 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzipereka chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa yayimuna iliyonse muzipereka makilogalamu awiri.
3 Com cada touro novo, ofereçam três quilos da melhor farinha misturada com azeite. Com cada carneiro, ofereçam dois quilos de farinha misturada com azeite
4 Pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja muzipereka kilogalamu imodzi.
4 e, com cada carneirinho, um quilo.
5 Muziperekanso mbuzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu.
5 Ofereçam a Deus também um bode como sacrifício para tirar os pecados do povo.
6 Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.
6 Tragam isso, além da oferta que é completamente queimada em sacrifício no primeiro dia do mês, junto com a sua oferta de cereais, e além da oferta que é completamente queimada todos os dias, junto com a oferta de cereais e a oferta de vinho que a acompanha. Essas ofertas de alimento têm um cheiro agradável ao Senhor .
7 “ ‘Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiriwu, muzichita msonkhano wopatulika. Muzisala zakudya ndipo musamagwire ntchito.
7 — No dia dez do sétimo mês vocês se reunirão para adorar a Deus. Nesse dia não comam nada e não trabalhem.
8 Muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma lokondweretsa Yehovayo; ngʼombe yayimuna imodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi. Zimenezi zizikhala zopanda chilema.
8 Deem a Deus, o Senhor , uma oferta que será completamente queimada em sacrifício e que tem um cheiro agradável a ele. Esse sacrifício será de um touro novo, um carneiro e sete carneirinhos de um ano, todos sem defeito.
9 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri;
9 Com cada touro novo, ofereçam três quilos da melhor farinha misturada com azeite. Com cada carneiro, ofereçam dois quilos de farinha misturada com azeite
10 kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiriwo.
10 e, com cada carneirinho, um quilo.
11 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo ija, kuwonjezanso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi cha chakumwa.
11 Ofereçam também um bode como sacrifício para tirar os pecados, além do bode que é oferecido para purificar o povo e além do sacrifício que é queimado e que é oferecido todos os dias, junto com a oferta de cereais e a oferta de vinho que o acompanha.
12 “ ‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri.
12 — No dia quinze do sétimo mês vocês se reunirão para adorar a Deus. Essa festa em honra do Senhor Deus deverá durar sete dias.
13 Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
13 No primeiro dia da festa tragam ao Senhor uma oferta de alimento que tem um cheiro agradável a ele. Essa oferta será de treze touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito.
14 Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri.
14 Com cada touro novo, ofereçam três quilos da melhor farinha misturada com azeite. Com cada carneiro, ofereçam dois quilos de farinha misturada com azeite
15 Pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa aamuna khumi ndi anayiwo, muzipereka chakudya cha kilogalamu imodzi.
15 e, com cada carneirinho, um quilo, junto com as ofertas de vinho que acompanham essa oferta.
16 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
16 Ofereçam também um bode como sacrifício para tirar os pecados do povo. Ofereçam isso, além do sacrifício que é completamente queimado todos os dias, junto com a oferta de cereais e a oferta de vinho que o acompanha.
17 “ ‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema.
17 — No segundo dia ofereçam doze touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
18 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
18 — ausente —
19 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
19 — ausente —
20 “ ‘Pa tsiku lachitatu muzipereka ngʼombe zazimuna khumi ndi imodzi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
20 — No terceiro dia ofereçam onze touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
21 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
21 — ausente —
22 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
22 — ausente —
23 “ ‘Pa tsiku lachinayi muzipereka ngʼombe zazimuna khumi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
23 — No quarto dia ofereçam dez touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
24 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
24 — ausente —
25 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
25 — ausente —
26 “ ‘Pa tsiku lachisanu muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zinayi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
26 — No quinto dia ofereçam nove touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
27 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
27 — ausente —
28 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
28 — ausente —
29 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zitatu, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
29 — No sexto dia ofereçam oito touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
30 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
30 — ausente —
31 Muziperekenso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
31 — ausente —
32 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa amuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
32 — No sétimo dia ofereçam sete touros novos, dois carneiros e catorze carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
33 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
33 — ausente —
34 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
34 — ausente —
35 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
35 — No oitavo dia vocês se reunirão para adorar a Deus, e ninguém trabalhará.
36 Muzipereka chopereka chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ngʼombe imodzi yayimuna, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa amuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
36 Ofereçam a Deus, o Senhor , um sacrifício que será completamente queimado, como uma oferta de alimento que tem um cheiro agradável a ele. Essa oferta será de um touro novo, um carneiro e sete carneirinhos de um ano, todos sem defeito. Junto com eles, deem também as outras ofertas que são exigidas para o primeiro dia.
37 Pamodzi ndi ngʼombe yayimunayo, nkhosa yayimunayo ndi ana ankhosawo, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
37 — ausente —
38 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
38 — ausente —
39 “ ‘Kuwonjezera pa zopereka zimene munalumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu, muzipereka zimenezi kwa Yehova pa masiku osankhika a chikondwerero chanu. Nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.’ ”
39 — São essas as leis a respeito dos sacrifícios que são completamente queimados, das ofertas de cereais, das ofertas de vinho e das ofertas de paz que vocês devem dar a Deus, o Senhor , nas datas marcadas para as festas. Essas coisas vocês devem oferecer a Deus e mais as ofertas que vocês prometerem ou as ofertas que fizerem por vontade própria.
40 Mose anawuza Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamulira.
40 Assim, Moisés disse aos israelitas tudo o que o Senhor lhe havia ordenado.
Atalhos do teclado
- Capítulo anterior←
- Próximo capítulo→
- Versículo anteriork
- Próximo versículoj
- Limpar seleçãoEsc
- Esta ajuda?