1 Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa.
2 Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.
3 Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ”
4 “Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:
5 Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?
6 Ine ndinatchera khutu kumvetsera
7 Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa
8 “ ‘Inu mukunena bwanji kuti,
9 Anthu anzeru achita manyazi;
10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena
11 Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga
12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?
13 “ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,
14 Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?
15 Tinkayembekezera mtendere
16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani
17 Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,
18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,
19 Imvani kulira kwa anthu anga
20 “Nthawi yokolola yapita,
21 Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;
22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?