1 Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:
2 Kuchokera kwa ana a Asafu:
3 Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake:
4 Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake:
5 Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.
6 Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.
7 Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.
8 Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.
9 Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe,
10 Maere achitatu anagwera Zakuri,
11 Maere achinayi anagwera Iziri,
12 Maere achisanu anagwera Netaniya,
13 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya,
14 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela,
15 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya,
16 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya,
17 Maere a khumi anagwera Simei,
18 Maere a 11 anagwera Azareli,
19 Maere a 12 anagwera Hasabiya,
20 Maere a 13 anagwera Subaeli,
21 Maere a 14 anagwera Matitiya,
22 Maere a 15 anagwera Yeremoti,
23 Maere a 16 anagwera Hananiya,
24 Maere a 17 anagwera Yosibakasa,
25 Maere a 18 anagwera Hanani,
26 Maere a 19 anagwera Maloti,
27 Maere a 20 anagwera Eliyata,
28 Maere a 21 anagwera Hotiri,
29 Maere a 22 anagwera Gidaliti,
30 Maere a 23 anagwera Mahazioti,
31 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri,