Números 26

NYA

1 Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni,

2 “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.”

3 Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,

4 “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.”

5 Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi:

6 kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;

7 Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.

8 Mwana wa Palu anali Eliabu,

9 ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova.

10 Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.

11 Koma ana a Kora sanafe nawo.

12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi:

13 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera;

14 Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.

15 Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi:

16 kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini;

17 kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi;

18 Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.

19 Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.

20 Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi:

21 Zidzukulu za Perezi zinali izi:

22 Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.

23 Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi:

24 kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu.

25 Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.

26 Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi:

27 Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.

28 Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:

29 Zidzukulu za Manase:

30 Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi;

31 kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli;

32 kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida;

33 (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)

34 Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.

35 Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi;

36 Zidzukulu za Sutela zinali izi:

37 Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500.

38 Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi:

39 kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu;

40 Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi:

41 Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.

42 Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi:

43 Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.

44 Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi:

45 ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya:

46 (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera)

47 Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.

48 Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi:

49 kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri;

50 Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.

51 Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.

52 Yehova anawuza Mose kuti,

53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo.

54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.

55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo.

56 Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”

57 Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa:

58 Awanso anali mabanja a Alevi:

59 Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo.

60 Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.

61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).

62 Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.

63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko.

64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;

65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Ler em outra tradução

Comparar lado a lado