Neemias 7

NYA

1 Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa.

2 Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.

3 Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

4 Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.

5 Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

6 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.

7 Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

8 Zidzukulu za Parosi

9 Zidzukulu za Sefatiya

10 Zidzukulu za Ara

11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)

12 Zidzukulu za Elamu

13 Zidzukulu za Zatu

14 Zidzukulu za Zakai

15 Zidzukulu za Binuyi

16 Zidzukulu za Bebai

17 Zidzukulu za Azigadi

18 Zidzukulu za Adonikamu

19 Zidzukulu za Abigivai

20 Zidzukulu za Adini

21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)

22 Zidzukulu za Hasumu

23 Zidzukulu za Bezayi

24 Zidzukulu za Harifu

25 Zidzukulu za Gibiyoni

26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa

27 Anthu a ku Anatoti

28 Anthu a ku Beti-Azimaveti

29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti

30 Anthu a ku Rama ndi Geba

31 Anthu a ku Mikimasi

32 Anthu a ku Beteli ndi Ai

33 Anthu a ku Nebo winayo

34 Ana a Elamu wina

35 Zidzukulu za Harimu

36 Zidzukulu za Yeriko

37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono

38 Zidzukulu za Senaya

39 Ansembe anali awa:

40 Zidzukulu za Imeri

41 Zidzukulu za Pasi-Huri

42 Zidzukulu za Harimu

43 Alevi anali awa:

44 Anthu oyimba:

45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni

48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,

49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,

50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,

51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,

52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,

53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,

54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,

55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema

56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

57 Zidzukulu za antchito a Solomoni:

58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,

59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu

60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo

61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

62 Zidzukulu za

63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.

65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360.

67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245.

68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245.

69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.

71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250.

72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ler em outra tradução

Comparar lado a lado