Jeremias 17

NYA

1 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,

2 Ngakhale ana awo amakumbukira

3 Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense

4 Mudzataya dziko limene ndinakupatsani

5 Yehova akuti,

6 Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;

7 “Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,

8 Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi

9 Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse

10 “Ine Yehova ndimafufuza mtima

11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo

12 Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero

13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,

14 Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;

15 Anthu akumandinena kuti,

16 Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.

17 Musandichititse mantha;

18 Ondizunza anga achite manyazi,

19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu.

20 Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’

21 Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu.

22 Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu.

23 Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga.

24 Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli.

25 Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya.

26 Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova.

27 Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”

Ler em outra tradução

Comparar lado a lado