1 Ndidzamuyimbira bwenzi langa
2 Anatipula nachotsa miyala yonse
3 “Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,
4 Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa
5 Tsopano ndikuwuzani
6 Ndidzawusandutsa tsala,
7 Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse
8 Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,
9 Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti,
10 Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,
11 Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa
12 Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,
13 Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo
14 Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta
15 Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.
17 Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;
18 Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,
19 amene amanena kuti, “Yehova afulumire,
20 Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino
21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru
22 Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo
23 amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu
24 Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu
25 Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;
26 Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,
27 Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,
28 Mivi yawo ndi yakuthwa,
29 Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,
30 Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula