1 Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri.
2 Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye.
3 Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
4 Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.
5 Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati,
6 Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati,
7 Iye ponena za angelo akuti,
8 Koma za Mwana wake akuti,
9 Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
10 Mulungu akutinso,
11 Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire.
12 Mudzazipindapinda ngati chofunda;
13 Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti,
14 Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?