1 Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.
2 Ana aamuna a Yafeti anali:
3 Ana aamuna a Gomeri anali:
4 Ana aamuna a Yavani anali:
5 (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).
6 Ana aamuna a Hamu anali:
7 Ana aamuna a Kusi anali:
8 Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
9 Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
10 Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
11 Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,
12 ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
13 Igupto ndiye kholo la
14 Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
15 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,
16 Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
17 Ahivi, Aariki, Asini,
18 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
19 mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20 Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
21 Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
22 Ana aamuna a Semu anali:
23 Ana aamuna a Aramu anali:
24 Aripakisadi anabereka Sela,
25 A Eberi anabereka ana aamuna awiri:
26 Yokitani anabereka
27 Hadoramu, Uzali, Dikila,
28 Obali, Abimaeli, Seba,
29 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
30 Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
32 Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.