Apocalipse 18

NYA

1 Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero.

2 Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:

3 Pakuti mayiko onse amwa

4 Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:

5 pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,

6 Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.

7 Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri

8 Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;

9 “Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake.

10 Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.

11 “Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo,

12 katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira;

13 zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.

14 “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’

15 Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro

16 ndipo adzalira mokuwa kuti,

17 Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’

18 Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’

19 Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,

20 “Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!

21 Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,

22 Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,

23 Kuwala kwa nyale

24 Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,

Ler em outra tradução

Comparar lado a lado